Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 32:25-37 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Pabwalo lupanga lidzalanda,Ndi m'zipinda mantha;Lidzaononga mnyamata ndi namwali,Woyamwa pamodzi ndi munthu waimvi.

26. Ndinati, Ndikadawauzira ndithu,Ndikadafafaniza cikumbukiro cao mwa anthu;

27. Ndikadapanda kuopa mkwiyo wapamdani,Angayese molakwa outsana nao,Anganene, Lakwezeka dzanja lathu,Ndipo Yehova sanacita ici conse.

28. Popeza iwo ndiwo mtundu wa anthu wosowa uphungu konse,Ndipo alibe cidziwitso.

29. Akadakhala nazo nzeru, akadazindikira ici,Akadasamalira citsirizo cao!

30. Mmodzi akadapitikitsa zikwi,Awiri akadathawitsa zikwi khumi,Akadapanda kuwagulitsa Thanthwelao,Akadapanda kuwapereka Yehova.

31. Popeza thanthwe lao nlosanga Thanthwe lathu,Oweruza a pamenepo ndiwo adani athu.

32. Pakuti mpesa wao ndiwo wa ku Sodomu,Ndi wa m'minda ya ku Gomora;Mphesa zao ndizo mphesa zandulu,Matsangwi ao ngowawa.

33. Vinyo wao ndiwo ululu wa zinjoka,Ndi ululu waukali wa mphiri.

34. Kodi sicisungika ndi Ine,Colembedwa cizindikilo mwa cuma canga ceni ceni?

35. Kubwezera cilango nkwanga, kubwezera komwe,Pa nyengo ya kuterereka phazi lao;Pakuti tsiku la tsoka lao layandika,Ndi zinthu zowakonzeratu zifulomira kudza.

36. Popeza Yehova adzaweruza anthuace,Nadzacitira nsoni anthu ace;Pakuona iye kuti mphamvu yao yatha,Wosatsala womangika kapena waufulu,

37. Pamenepo adzati, Iri kuti milunguyao,Thanthwe limene anathawirako?

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 32