Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 31:24-27 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

24. Ndipo kunali, Mose atatha kulembera mau a cilamulo ici m'buku, kufikira atalembera onse,

25. Mose anauza Alevi akunyamula likasa la cipangano la Yehova, ndi kuti,

26. Landirani buku ili la cilamulo, nimuliike pambali pa likasa la cipangano la Yehova Mulungu wanu, likhale komweko mboni yakutsutsa inu.

27. Pakuti ndidziwa kupikisana kwanu, ndi kupulukira kwanu; taonani, pokhala ndikali ndi moyo pamodzi ndi inu lero, mwapikisana ndi Yehova: koposa kotani nanga nditamwalira ine!

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 31