Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 29:4-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

4. koma Yehova sanakupatsani mtima wakudziwa, ndi maso akupenya, ndi makutu akumva, kufikira lero lino.

5. Ndipo ndinakutsogolerani zaka makumi anai m'cipululu; zobvala zanu sizinatha pathupi panu, ndi nsapato zanu sizinatha pa phazi lanu.

6. Simunadya mkate, simunamwa vinyo kapena cakumwa colimba; kuti mudziwe kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu.

7. Ndipo pamene munafika pamalo pano, Sihoni mfumu ya Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basana, anaturuka kudzakomana nafe kunkhondo, ndipo tinawakantha;

8. ndipo tinalanda dziko lao, ndi kulipereka likhale colowa cao ca Arubeni, ndi Agadi, ndi pfuko la hafu la Manase.

9. Cifukwa cace sungani mau a cipangano ici ndi kuwacita, kuti mucite mwanzeru m'zonse muzicita.

10. Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mapfuko anu, akuru anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israyeli;

11. makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi;

12. kuti mulowe cipangano ca Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lace, limene Yehova Mulungu wanu acita ndi inu lero lino;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 29