Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 29:10-26 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Muimirira inu nonse lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wanu; mafumu anu, mapfuko anu, akuru anu, ndi akapitao anu, amuna onse a Israyeli;

11. makanda anu, akazi anu, ndi mlendo wanu wakukhala pakati pa zigono zanu, kuyambira wotema nkhuni kufikira wotunga madzi;

12. kuti mulowe cipangano ca Yehova Mulungu wanu, ndi lumbiriro lace, limene Yehova Mulungu wanu acita ndi inu lero lino;

13. kuti adzikhazikire inu, mtundu wace wa anthu lero lino, ndi kuti akhale kwa inu Mulungu, monga ananena ndi inu, ndi monga analumbirira makolo anu, Abrahamu, Isake, ndi Yakobo.

14. Koma sindicita cipangano ici ndi lumbiro ili ndi inu nokha;

15. komanso ndi iye wakuimirira pano nafe lero lino pamaso pa Yehova Mulungu wathu, ndiponso ndi iye wosakhala pano nafe lero lino.

16. Pakuti mudziwa cikhalidwe cathu m'dziko la Aigupto, ndi kuti tinapyola pakati pa amitundu amene munawapyola;

17. ndipo munapenya zonyansa zao, ndi mafano ao, mtengo ndi mwala, siliva ndi golidi, zokhala pakati pao;

18. kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena pfuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi cowawa.

19. Ndipo kungakhale, akamva mau a lumbiro ili adzadzidalitsa m'mtima mwace, ndi kuti, Ndidzakhala nao mtendere, ndingakhale ndiyenda nao mtima wanga wopulukira, kuledzera nditamva ludzu;

20. Yehova sadzamkhululukira, koma pamenepo mkwiyo wa Yehova ndi nsanje yace zidzamfukira munthuyo; ndipo temberero lonse lolembedwa m'buku ili lidzamkhalira; ndipo Yehova adzafafaniza dzina lace pansi pa thambo.

21. Ndipo Yehova adzamsiyanitsa ndi mafuko onse a Israyeli ndi kumcitira coipa, monga mwa matemberero onse a cipangano colembedwa m'buku ili la cilamulo.

22. Ndipo mbadwo ukudza, ana anu akuuka mutafa inu, ndi mlendo wocokera ku dziko lakutali, adzati, pakuona iwo miliri ya dziko ili, ndi nthendazi; Yehova awadwalitsa nazo,

23. ndi kuti lidapsa dziko lace lonse ndi sulfure, ndi mcere, kuti sabzalamo, kapena siliphukitsa kanthu kapena sumerapo msipu, monga kupasula kwace kwa Sodomu ndi Gomora, Adima, ndi Zeboimu, imene Yehova anaipasula m'mkwiyo wace ndi ukali wace;

24. inde amitundu onse adzati, Yehova anacitira dziko ili cotero cifukwa ninji? nciani kupsa mtima kwakukuru kumene?

25. Pamenepo adzati, Popeza analeka cipangano ca Yehova, Mulungu wa makolo ao, cimene anacita nao pakuwaturutsa m'dziko la Aigupto;

26. napita natumikira milungu yina, naigwadira, milungu imene sanaidziwa, imene sanawagawira;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 29