Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:29-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.

30. Mudzaparana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzanka munda wamphesa, osalawa zipatso zace.

31. Adzapha ng'ombe yanu pamaso panu, osadyako inu; adzalanda buru wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.

32. Adzapereka ana anu amuna ndi akazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.

33. Mtundu wa anthu umene simudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi nchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28