Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:27-33 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

27. Yehova adzakukanthani ndi zirombo za ku Aigupto, ndi nthenda yoturuka mudzi, ndi cipere, ndi mphere, osacira nazo.

28. Yehova adzakukanthani ndi misala, ndi khungu, ndi kuzizwa mumtima;

29. ndipo mudzafufuza usana, monga wakhungu amafufuza mumdima, ndipo simudzapindula nazo njira zanu; koma mudzakhala wopsinjika, nadzakuberani masiku onse, wopanda wina wakukupulumutsani.

30. Mudzaparana ubwenzi ndi mkazi, koma mwamuna wina adzagona naye; mudzamanga nyumba, osakhala m'mwemo; mudzanka munda wamphesa, osalawa zipatso zace.

31. Adzapha ng'ombe yanu pamaso panu, osadyako inu; adzalanda buru wanu molimbana pamaso panu, osakubwezerani; adzapereka nkhosa zanu kwa adani anu, wopanda wina wakukupulumutsani.

32. Adzapereka ana anu amuna ndi akazi kwa anthu a mtundu wina, ndipo m'maso mwanu mudzada ndi kupenyerera, powalirira tsiku lonse; koma mulibe mphamvu m'dzanja lanu.

33. Mtundu wa anthu umene simudziwa udzadya zipatso za nthaka yanu ndi nchito zanu zonse; ndipo mudzakhala wopsinjika ndi wophwanyika masiku onse;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28