Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:21-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

21. Yehova adzakumamatiritsani mliri kufikira akakuthani kukucotsani kudziko, kumene mupitako kulilandira.

22. Yehova adzakukanthani ndi nthenda yoondetsa ya cifuwa, ndi malungo, ndi cibayo, ndi kutentha thupi, ndi lupanga, cinsikwi ndi cinoni; ndipo zidzakutsatani kufikira mwatayika.

23. Ndipo thambo lanu la pamwamba pamutu panu lidzakhala ngati mkuwa, ndi dziko liri pansi panu ngati citsulo.

24. Yehova adzasanduliza mvula ya dziko lanu ikhale pfumbi ndi phulusa; zidzakutsikirani kucokera kumwamba, kufikira mwaonongeka.

25. Yehova adzalola adani anu akukantheni; mudzawaturukira njira imodzi, koma mudzawathawa pamaso pao njira zisanu ndi ziwiri, ndipo mudzagwedezeka pakati pa maufumu onse a dziko lapansi.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28