Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 28:1-9 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kudzali, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu mwacangu, ndi kusamalira kucita malamulo ace onse amene ndikuuzani lero, kuti Yehova Mulungu wanu adzakukulitsani koposa amitundu onse a pa dziko lapansi;

2. ndipo madalitso awa onse adzakugwerani, ndi kukupezani, mukadzamvera mau a Yehova Mulungu wanu.

3. Mudzakhala odala m'mudzi, ndi odala kubwalo.

4. Zidzakhala zodala zipatso za thupi lanu, ndi zipatso za nthaka yanu, ndi zipatso za zoweta zanu, zoswana za ng'ombe zanu, ndi zoswana za nkhosa zanu.

5. Zidzakhala zodala mtanga wanu, ndi coumbiramo mkate wanu.

6. Mudzakhala odala polowa inu, mudzakhala odala poturuka inu.

7. Yehova adzakantha adani anu akukuukirani; adzakudzerani njira imodzi, koma adzathawa pamaso panu njira zisanu ndi ziwiri.

8. Yehova adzakulamulirani dalitso m'nkhokwe zanu, ndi m'zonse muturutsirako dzanja lanu; ndipo adzakudalitsani m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani,

9. Yehova adzakukhazikirani yekha mtundu wa anthu wopatulika, monga anakulumbirirani; ngati mudzasunga malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kuyenda m'njira zace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 28