Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 27:1-12 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo Mose ndi akuru a Israyeli anauza anthu, nati, Sungani malamulo onse ndikuuzani lero.

2. Ndipo kudzali, tsiku lakuoloka inu Yordano kulowa dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, kuti mudziutsire miyala yaikuru, ndi kuimata ndi njeresa;

3. ndipo mulemberepo mau onse a cilamulo ici, mutaoloka; kuti mulowe m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi, monga Yehova Mulungu wa makolo anu ananena ndi inu.

4. Ndipo kudzali, mutaoloka Yordano, muutse miyala iyi ndikuuzani lero, m'phiri la Ebala, ndi kuimata ndi njeresa.

5. Ndipo komweko mumangire Yehova Mulungu wanu guwa la nsembe, guwa la nsembe lamiyala; musakwezepo cipangizo cacitsulo.

6. Mumange guwa la nsembe la Yehova Mulungu wanu lamiyala yosasema; ndi kuperekapo nsembe zopsereza kwa Yehova Mulungu wanu;

7. ndi kuphera nsembe zoyamika, ndi kudyapo, ndi kukondwera pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

8. Ndipo mulembere pa miyalayi mau onse a cilamulo ici mopenyeka bwino.

9. Ndipo Mose, ndi ansembe Alevi ananena ndi Israyeli wonse, ndi kuti, Khalani cete, imvanitu, Israyeli; lero lino mwasanduka mtundu wa anthu wa Yehova Mulungu wanu.

10. Potero muzimvera mau a Yehova Mulungu wanu, ndi kucita malamulo ace, ndi malemba ace, amene ndikuuzani lero lino.

11. Ndipo Mose anauza anthu tsiku lomwelo, ndi kuti,

12. Aimirire awa pa phiri la Gerizimu kudalitsa anthu, mutaoloka Yordano: Simeoni ndi Levi, ndi Yuda, ndi Isakara, ndi Yosefe, ndi Benjamini.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 27