Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 26:11-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

11. ndipo mukondwere nazo zokoma zonse zimene Yehova Mulungu wanu akupatsani, inu ndi nyumba zanu, inu ndi Mlevi, ndi mlendo ali pakati panu.

12. Mutatha kugawa magawo khumi, zobala zanu zonse caka cacitatu, ndico caka cogawa magawo khumi, muzizipereka kwa Mlevi, kwa mlendo, kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, kuti adye m'midzi mwanu, ndi kukhuta.

13. Ndipo munene pamaso pa Yehova Mulungu wanu, Ndacotsa zopatulika m'nyumba mwanga, ndi kuzipereka kwa Mlevi, ndi kwa mlendo, ndi kwa mwana wamasiye, ndi kwa mkazi wamasiye, monga mwa lamulo lanu lonse munandilamulira ine; sindinalakwira malamulo anu, kapena kuwaiwala.

14. Sindinadyako m'cisoni canga, kapena kucotsako podetsedwa, kapena kuperekako kwa akufa; ndamvera mau a Yehova Mulungu wanga; ndacita monga mwa zonse munandilamulira ine.

15. Penyani muli mokhalamo mwanu mopatulika, m'mwamba, ndipo dalitseni anthu anu Israyeli, ndi nthaka imene munatipatsa, monga munalumbirira makolo athu, dziko moyenda mkaka ndi uci ngati madzi.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 26