Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 25:14-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Musamakhala nayo m'nyumba yanu miyeso ya efa yosiyana, waukuru ndi waung'ono.

15. Muzikhala nao mwala wa muyeso wofikira ndi woyenera; mukhale nao muyeso wa efa wofikira ndi woyenera; kuti masiku anu acuruke m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.

16. Pakuti onse akucita zinthu izi, onse akucita cisalungamo, Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

17. Kumbukilani cocitira inu Amaleki panjira, poturuka inu m'Aigupto;

18. kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofok a akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaopa Mulungu,

19. Ndipo kudzali, pamene Yehova Mulungu wanu atakupumulitsirani adani anu onse ozungulira, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale colowa canu canu, kuti muzifafaniza cikumbutso ca Amaleki pansi pa thambo; musamaiwala.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 25