Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 24:10-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Mukakongoletsa mnansi wanu ngongole iri yonse, musamalowa m'nyumba mwace kudzitengera cikole cace.

11. Muime pabwalo, ndi munthu amene umkongoletsayo azituruka naco cikoleco kwa inu muli pabwalo.

12. Ndipo akakhala munthu waumphawi musagone muli naco cikole cace;

13. polowa dzuwa mumbwezeretu cikoleco, kuti agone m'cobvala cace, ndi kukudalitsani; ndipo kudzakukhalirani cilungamo pamaso pa Yehova Mulungu wanu.

14. Musamasautsa wolembedwa nchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu.

15. Pa tsiku lace muzimpatsa kulipira kwace, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wace ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhaireni cimo.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 24