Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 23:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pakakhala munthu pakati pa inu, ndiye wosayera cifukwa cocitika usiku, azituruka kunja kwa cigono, asalowe pakati pa cigono;

11. koma kudzali pofika madzulo, asambe m'madzi; ndipo litalowa dzuwa alowe pakati pa cigono.

12. Mukhale nao malo kunja kwa cigono kumene muzimukako kuthengo;

13. nimukhale naco cokumbira mwa zida zanu; ndipo kudzali, pakukhala inu pansi kuthengo mukumbe naco, ndi kutembenuka ndi kufotsera cakuturukaco;

14. popeza Yehova Mulungu wanu ayenda pakati pa cigono canu, kukupulumutsani ndi kupereka adani anu pamaso panu; cifukwa cace cigono canu cikhale copatulika; kuti angaone kanthu kodetsa mwa inu, ndi kukupotolokerani.

15. Musamapereka kwa mbuye wace kapolo wopulumuka kwa mbuye wace kuthawira kwa inu;

16. akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m'mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.

17. Pasakhale mkazi wacigololo pakati pa ana akazi a Israyeli, kapena wacigololo pakati pa ana amuna a Israyeli.

18. Musamabwera nayo mphotho ya wacigololo, kapena mtengo wace wa garu kulowa nazo m'nyumba ya Yehova Mulungu wanu, cifukwa ca cowinda ciri conse; pakuti onse awiriwa Yehova Mulungu wanu anyansidwa nao.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 23