Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 22:9-16 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

9. Musamabzala mbeu zosiyana m'munda wanu wamphesa, kuti zingaipsidwe mbeu zonse udazibzala, ndi zipatso za munda wamphesa zomwe.

10. Musamalima ndi buru ndi ng'ombe zikoke pamodzi.

11. Musamabvala nsaru yosokonezeka yaubweya pamodzi ndi thonje.

12. Mudzipangire mphonje pa ngondya zinai za copfunda canu cimene mudzipfunda naco.

13. Munthu akatenga mkazi, nalowana naye, namuda,

14. namneneza zoutsa mbiri yamanyazi, ndi kumveketsa dzina loipa, ndi kuti, Ndinamtenga mkazi uyu, koma polowana nave sindinapeza zizindikilo zakuti ndiye namwali ndithu;

15. pamenepo atate wa namwaliyo ndi mai wace azitenga ndi kuturuka nazo zizindikilo za unamwali wace wa namwaliyo, kumka nazo kwa akuru a mudzi kucipata;

16. ndipo atate wa namwaliyo azinena kwa akuru, Ndinampatsa munthuyu mwana wanga wamkazi akhale mkazi wace, koma amuda;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 22