Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 22:23-30 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Pakakhala namwali, wosadziwa mwamuna, wopalidwa ubwenzi ndi mwamuna, ndipo anampeza m'mudzi mwamuna, nagona nave;

24. muziwaturutsa onse awiri kumka nao ku cipata ca mudzi uwo, ndi kuwaponya miyala kuti afe; namwaliyo popeza sanapfuula angakhale anali m'mudzi; ndi mwamuna popeza anacepetsa mkazi wa mnansi wace; cotero muzicotsa coipaco pakati panu.

25. Koma mwamuna akapeza namwali wopalidwa bwenzi kuthengo, namgwira mwamunayo, nagona naye; pamenepo afe mwamuna yekha wogona naye;

26. koma namwaliyo musamamcitira kanthu; namwaliyo alibe cimo loyenera imfa; pakuti mlandu uwu ukunga munthu waukira mnzace namupha;

27. pakuti anampeza kuthengo; namwali wopalidwa bwenziyo anapfuula, koma panalibe wompulumutsa.

28. Munthu akapeza namwali wosadziwa mwamuna, ndiye wosapalidwa ubwenzi, oakamgwira nagona naye, napezedwa iwo,

29. pamenepo mwamuna amene anagona naye azipatsa atate wace wa namwaliyo masekeli makumi asanu a siliva, ndipo azikhala mkazi wace; popeza anamcepetsa; sakhoza kumcotsa masiku ace onse.

30. Munthu asatenge mkazi wa atate wace, kapena kubvula atate wace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 22