Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 22:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Mukapenya ng'ombe kapena nkhosa ya mbale wako zirikusokera musamazilekerera, muzimbwezera mbale wanu ndithu.

2. Ndipo ngati mbale wanu sakhala pafupi ndi inu, kapena mukapanda kumdziwa, mubwere nayo kwanu ku nyumba yanu, kuti ikhale kwanu, kufikira mbale wanu akaifuna, ndipo wambwezera iyo.

3. Mutero nayenso buru wace; mutero naconso cobvala cace; mutero naconso cotayika ciri conse ca mbale wanu, cakumtayikira mukacipeza ndi inu; musamazilekerera.

4. Mukapenya buru kapena ng'ombe ya mbale wanu, zitagwa m'njira, musamazilekerera; mumthandize ndithu kuziutsanso.

5. Mkazi asabvale cobvala ca mwa muna, kapena mwamuna asabvale cobvala ca mkazi; pakuti ali yense wakucita izi Yehova Mulungu wanu anyansidwa naye.

6. Mukacipeza cisa ca mbalame panjira, mumtengo kapena panthaka pansi, muli ana kapena mazira, ndi mace alikuumatira ana kapena mazira, musamatenga mace pamodzi ndi ana;

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 22