Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 21:10-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Pamene muturuka kumka ku nkhondo ya pa adani anu, ndipo Yehova Mulungu wanu awapereka m'manja mwanu, ndipo muwagwira akhale akapolo anu;

11. mukaona mwa akapolowa mkazi wokongola, mukamkhumba, ndi kufuna kumtenga akhale mkazi wanu;

12. pamenepo mufike naye kwanu ku nyumba yanu; ndipo amete tsitsi la pamutu pace, ndi kuwenga makadabo ace;

13. nabvule zobvala za ukapolo wace, nakhale m'nyumba mwanu, nalire atate wace, ndi mai wace mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wace, ndi iye akhale mkazi wanu.

14. Ndipo kudzali, mukapanda kukondwera naye, mumlole apite komwe afuna; koma musamgulitsa ndalama konse, musamamuyesa cuma, popeza wamcepetsa.

15. Munthu akakhala nao akazi awiri, wina wokondana naye, wina wodana naye, nakambalira ana, wokondana naye, ndi wodana naye yemwe; ndipo mwana wamwamuna woyamba akakhala wa iye uja anadana naye;

16. pamenepo kudzali, tsiku lakugawira ana ace amuna cuma cace, sangakhoze kuyesa mwana wa wokondana naye woyamba kubadwa, wosati mwana wa wodana naye, ndiye woyamba kubadwatu.

17. Koma azibvomereza wobadwa woyamba, mwana wa wodana naye, ndi kumwirikizira gawo lace la zace zonse; popeza iye ndiye ciyambi ca mphamvu yace; zoyenera woyamba kubadwa nzace.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 21