nabvule zobvala za ukapolo wace, nakhale m'nyumba mwanu, nalire atate wace, ndi mai wace mwezi wamphumphu; ndipo atatero mulowe naye ndi kukhala mwamuna wace, ndi iye akhale mkazi wanu.