Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 20:8-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

8. Pamenepo akapitao anenenso kwa anthu, ndi kuti, Munthuyo ndani wakucita mantha ndi wofumuka mtima? amuke nabwerere kunyumba kwace, ingasungunuke mitima ya abale ace monga mtima wace.

9. Ndipo kudzali, atatha akapitao kunena ndi anthu, aike akazembe a makamu atsogolere anthu.

10. Pamene muyandikiza mudzi kucita nao nkhondo, muziupfuulira ndi mtendere.

11. Ndipo kudzali, ukakubwezerani mau a mtendere, ndi kukutsegulirani, pamenepo anthu onse opereka m'mwemo akhale alambi anu, nadzakutumikirani.

12. Koma ukapanda kucita zamtendere ndi inu, koma kucita nkhondo nanu, pamenepo uumangire tsasa.

13. Ndipo pamene Yehova Mulungu wanu aupereka m'dzanja lanu, mukanthe amuna ace onse ndi lupanga lakuthwa.

14. Koma akazi ndi ana ndi ng'ombe ndi zonse ziti m'mudzimo, zankhondo zace zonse, mudzifunkhire nokha; ndipo mudye zankhondo za adani anu, zimene Yehova Mulungu wanu anakupatsani.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 20