13. Diso lanu lisamcitire cifundo, koma mucotse mwazi wosacimwa m'Israyeli, kuti cikukomereni.
14. Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'colowa canu mudzalandiraci, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.
15. Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iri yonse, kapena cimo liri lonse adalicimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.
16. Mboni yaciwawa ikaukira munthu kumneneza ndi kuti analakwa;
17. pamenepo anthu onse awiri, pakati pao pali makaniwo, aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza okhala m'masiku awa;
18. ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wace;
19. mumcitire monga iye anayesa kumcitira mbale wace; motero mucotse coipaco pakati panu.