Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 19:12-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. pamenepo akuru a mudzi wace atumize ndi kumtengako ndi kumpereka m'manja mwa wolipsa mwazi, kuti afe.

13. Diso lanu lisamcitire cifundo, koma mucotse mwazi wosacimwa m'Israyeli, kuti cikukomereni.

14. Musamasendeza malire a mnansi wanu, amene adawaika iwo a kale lomwe, m'colowa canu mudzalandiraci, m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani likhale lanu lanu.

15. Mboni imodzi isamaukira munthu pa mphulupulu iri yonse, kapena cimo liri lonse adalicimwa; pakamwa pa mboni ziwiri, kapena pakamwa pa mboni zitatu mlandu utsimikizike.

16. Mboni yaciwawa ikaukira munthu kumneneza ndi kuti analakwa;

17. pamenepo anthu onse awiri, pakati pao pali makaniwo, aziima pamaso pa Yehova, pamaso pa ansembe ndi oweruza okhala m'masiku awa;

18. ndipo oweruza afunsitse bwino; ndipo taonani, mboniyo ikakhala mboni yonama, yomnamizira mbale wace;

19. mumcitire monga iye anayesa kumcitira mbale wace; motero mucotse coipaco pakati panu.

20. Ndipo otsalawo adzamva, nadzaopa, ndi kusacitanso monga coipaco pakati panu.

21. Ndipo diso lanu lisacite cifundo, moyo kulipa moyo, diso kulipa diso, dzino kulipa dzino, dzanja kulipa dzanja, phazi kulipa phazi.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 19