Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 18:1-13 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ansembe Alevi, pfuko lonse la Levi, alibe gawo kapena colowa pamodzi ndi Israyeli; azizidya nsembe zamoto za Yehova, ndi colowa cace,

2. Alibe colowa pakati pa abale ao; Yehova mwini wace ndiye colowa cao, monga ananena nao.

3. Ndipo zoyenera ansembe, awapatse anthu akuphera nsembe ndizo: ingakhale ng'ombe kapena nkhosa azipatsa wansembe mwendo wamwamba, ndi ya m'masaya ndi chipfu.

4. Zipatso zoyamba za tirigu wanu, za vinyo wanu, ndi za mafuta anu ndi ubweya woyamba kuusenga, muwapatse izi.

5. Popeza Yehova Mulungu wanu anawasankha mwa mapfuko anu onse, aimirire natumikire m'dzina la Yehova, iwo ndi ana ao amuna kosalekeza.

6. Ndipo Mlevi akacokera ku mudzi wanu wina m'Israyeli monse, kumene akhalako, nakadza ndi cifuniro conse ca moyo wace ku malo amene Yehova adzasankha;

7. pamenepo azitumikira m'dzina la Yehova Mulungu wace, monga amacita abale ace onse Alevi akuimirirako pamaso pa Yehova.

8. Cakudya cao cizifanana, osawerengapo zolowa zace zogulitsa.

9. Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, musamaphunzira kucita mongamwa zonyansa za amitundu aja.

10. Asapezeke mwa inu munthu wakupitiriza mwana wace wamwamuna kapena mwana wace wamkazi ku mota wa ula, wosamalira mitambo, kapena wosamalira kulira kwa mbalame, kapena wanyanga.

11. Kapena wotsirika, kapena wobwebweta, kapena wopenduza, kapena wofunsira akufa.

12. Popeza ali yense wakucita izi Yehova anyansidwa naye; ndipo cifukwa ca zonyansa izi Yehova Mulungu wanu awapitikitsa pamaso panu.

13. Mukhale angwiro ndi Yehova Mulungu wanu.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 18