12. Koma munthu wakucita modzikuza, osamvera wansembe wokhala ciriri kutumikirako pamaso pa Yehova Mulungu wanu, kapena woweruza, munthuyo afe; ndipo mucotse coipaco kwa Israyeli.
13. Ndipo anthu onse adzamva ndi kucita mantha, osacitanso modzikuza.
14. Mutakalowa m'dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani, ndi kulilandira lanu lanu, ndi kukhalamo; ndipo mukanena, Tidziikire mfumu, monga amitundu onse akutizinga;
15. mumuiketu mfumu yanu imene Yehova Mulungu wanu adzaisankha; wina pakati pa abale anu mumuike mfumu yanu; simuyenera kudziikira mlendo, wosakhala mbale wanu.
16. Koma asadzicurukitsire akavalo iye, kapena kubwereretsa anthu amke ku Aigupto, kuti acurukitse akavalo; popeza Yehova anati nanu, Musamabwereranso njira iyi.
17. Ndipo asadzicurukitsire akazi, kuti ungapatuke mtinta wace; kapena asadzicurukitsire kwambiri siliva ndi golidi.
18. Ndipo kudzali, pakukhala iye pa mpando wacifumu wa ufumu wace, adzilemberere cofanana ca cilamuloici m'buku, acitenge pa ici ciri pamaso pa ansembe Alevi;