Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 14:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Inu ndinu ana a Yehova Mulungu wanu; musamadziceka, kapena kumeta tsitsi pakati pa maso cifukwa ca akufa.

2. Popeza ndinu mtundu wa anthu opatulikira Yehova Mulungu wanu, ndipo Yehova anakusankhani mukhale mtundu wa anthu wa pa wokha wa iye yekha, mwa mitundu yonse ya anthu okhala pankhope pa dziko lapansi.

3. Musamadya conyansa ciri conse,

4. Nyamazi muyenera kumadya ndi izi: ng'ombe, nkhosa, ndi mbuzi,

5. ngondo, ndi nswala ndi mphoyo, ndi mphalapala, ndi ngoma, ndi nyumbu, ndi mbalale.

6. Ndipo nyama iri yonse yogawanika ciboda, nikhala yogawanikadi ciboda, nibzikula, imeneyo muyenera kudya.

7. Koma izi zokha simuyenera kuzidya mwa zobzikulazo, kapena zogawanika ciboda: ngamila, ndi ka'ulu, ndi mbira, popezazibzikula, komazosagawanika ciboda, muziyese zodetsa;

8. ndi nkhumba, popeza igawanika ciboda koma yosabzikula, muiyese yodetsa; musamadya nyama yao, musamakhudza mitembo yao.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 14