Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 11:25-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

25. Palibe munthu adzaima paraaso panu; Yehova Mulungu wanu adzanjenjemeretsa ndi kuopsa dziko lonse mudzapondapo, cifukwa ca inu, monga ananena ndi inu.

26. Taonani, ndirikuika pamaso panu lero dalitso ndi temberero;

27. dalitso, ngati mudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikuuzani lero lino;

28. koma temberero, ngati simudzamvera malamulo a Yehova Mulungu wanu, ndi kupatuka m'njira ndikuuzani lero lino, kutsata milungu yina imene simunaidziwa.

29. Ndipo kudzakhala, atakulowetsani Yehova Mulungu wanu m'dziko limene mumkako kulilandira, munene mdalitso pa phiri la Gerizimu, ndi temberero pa phiri la Ebala.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 11