Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 11:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Cifukwa cace muzikonda Yehova Mulungu wanu, ndi kusunga cilangizo cace, ndi malemba ace, ndi maweruzo ace, ndi malamulo ace, masiku onse.

2. Ndipo dziwani lero lino; pakuti sindinena ndi ana anu osadziwa, ndi osapenya kulanga kwa Yehova Mulungu wanu, ukulu wace, dzanja lace lamphamvu, ndi mkono wace wotambasuka,

3. ndi zizindikilo zace, ndi nchito zace, adazicitira Farao mfumu ya Aigupto, ndi dziko lace lonse pakati pa Aigupto;

4. ndi cocitira iye nkhondo ya Aigupto, akavalo ao, ndi agareta ao; kuti anawamiza m'madzi a Nyanja Yofiira, muja anakutsatani m'mbuyo, ndi kuti Yehova anawaononga kufikira lero lino;

5. ndi cimene anakucitirani m'cipululu, kufikira munadza kumalo kuno;

6. ndi cimene anacitira Datani ndi Abiramu, ana a Eliabu, mwana wa Rubeni; muja nthaka inatsegula pakamwa pace, ndi kuwameza iwo, ndi mabanja ao, ndi mahema ao, ndi za moyo zonse zakuwatsata pakati pa Israyeli wonse.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 11