Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 1:41-46 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

41. Pamenepo munayankha ndi kunena ndi ine, Tacimwira Yehova, tidzakwera ndi kuthira mkhondo monga mwa zonse Yehova Mulungu wathu atiuza. Ndipo munadzimangira munthu yense zida zace za nkhondo, nimunakonzeka kukwera kumka kumapiri.

42. Koma Yehova anati kwa ine, Nena nao, Musakwerako, kapena kuthira nkhondo; popeza sindiri pakati panu; angakukantheni adani anu.

43. Pamene ndinanena ndi inu simunamvera; koma munatsutsana nao mau a Yehova ndi kucita modzikuza, nimunakwera kumka kumapiri.

44. Ndipo Aamori, akukhala m'mapiri muja, anaturuka kukomana ndi inu, nakupitikitsani, monga zimacita njuci, nakukanthani m'Seiri, kufikira ku Horima.

45. Ndipo munabwerera ndi kulira pamaso pa Yehova; koma Yehova sanamvera mau anu, kapena kukucherani khutu.

46. Potero munakhala m'Kadesi masiku ambiri, monga mwa masiku munakhalako.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 1