Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Deuteronomo 1:29-40 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

29. Pamenepo ndinati kwa inu, Musamaopsedwa, musamacita mantha nao.

30. Yehova Mulungu wanu wakutsogolera inu, iye adzathirira inu nkhondo, monga mwa zonse anakucitirani m'Aigupto pamaso panu;

31. ndi kucipululu, kumene munapenya kuti Yehova Mulungu wanu anakunyamulani, monga anyamula mwana wace wamwamuna, m'njira monse munayendamo, kufikira mutalowa m'malo muno.

32. Koma m'cinthu ici simunakhulupirira Yehova Mulungu wanu,

33. amene anakutsogolerani m'njira, kukufunirani malo akumanga mahema anu ndi mota usiku, kukuonetserani njira yoyendamo inu, ndi mumtambo usana.

34. Ndipo Yehova anamva mau a kunena kwanu, nakwiya, nalumbira, ndi kuti,

35. Palibe mmodzi wa anthu awa a mbadwo uno woipa adzaona dziko lokomalo ndinalumbira kupatsa makolo anuli.

36. Koma Kalebi mwana wa Yefune, iye adzaliona; ndidzampatsa iye dziko limene anapondapo, ndi ana ace; popeza analimbika ndi kutsata Yehova.

37. Yehova anakwiya ndi inenso cifukwa ca inu, ndi kuti, lwenso sudzalowamo.

38. Yoswa mwana wa Nuni, wakuima pamaso pako, iye adzalowamo; umlimbitse mtima; popeza iye adzalandiritsa Israyeli.

39. Ndipo ana anu amene mudanena, Adzakhala ogulidwa, ndi ana anu osadziwa cabwino kapena coipa ndi pano, iwo adzalowamo, ndidzawapatsa iwo ili, adzalilandira ndi iwo.

40. Koma inu, bwererani, mukani ulendo wanu kucipululu, njira ya ku Nyanja Yofiira.

Werengani mutu wathunthu Deuteronomo 1