Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 2:12-20 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. Cifukwa cace mfumu inakwiya, nizaza kwambiri, nilamulira kuti awaphe anzeru onse m'Babulo.

13. M'mwemo cilamuliroco cidamveka, ndi eni nzeru adati aphedwe; anafuna-funanso Danieli ndi anzace aphedwe.

14. Pamenepo Danieli anabweza mau a uphungu wanzeru kwa Arioki mkuru wa olindirira a mfumu, adaturukawo kukapha eni nzeru a ku Babulo;

15. anayankha nati kwa Arioki mkuru wa olindirira a mfumu, Cilamuliro ca mfumu cifulumiriranji? Pamenepo Arioki anadziwitsa Danieli cinthuci.

16. Nalowa Danieli, nafunsa mfumu amuikire nthawi, kuti aululire mfumu kumasulira kwace.

17. Pamenepo Danieli anapita ku nyumba kwace, nadziwitsa anzace Hananiya, Misaeli, ndi Azariya, cinthuci;

18. kuti apemphe zacifundo kwa Mulungu wa Kumwamba pa cinsinsi ici; kuti Danieli ndi anzace asaonongeke pamodzi ndi eni nzeru ena a ku Babulo.

19. Pamenepo cinsinsico cinabvumbulutsidwa kwa Danieli m'masomphenya a usiku. Ndipo Danieli analemekeza Mulungu wa Kumwamba.

20. Danieli anayankha, nati, Lilemekezedwe dzina la Mulungu ku nthawi za nthawi, a pakuti nzeru ndi mphamvu ziri zace;

Werengani mutu wathunthu Danieli 2