Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 11:39-45 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

39. Ndipo adzacita molimbana ndi malinga olimba koposa, pomthandiza mulungu wacilendo; ali yense wombvomereza adzamcurukitsira ulemu, nadzawacititsa ufumu pa ambiri, nadzagawa dziko mwa mtengo wace.

40. Ndipo nthawi yotsiriza mfumu ya kumwela idzalimbana naye, ndi mfumu ya kumpoto idzamdzera ngati kabvumvulu, ndi magareta, ndi apakavalo, ndi zombo zambiri; nadzalowa m'maiko, nadzasefukira ndi kupitirira.

41. Adzalowanso m'dziko lokometsetsalo ndi maiko ambiri adzapasuka; koma opulumuka dzanja lace ndi awa: Edomu, ndi Moabu, ndi oyamba a ana a Amoni.

42. Adzatambalitsiranso dzanja lace kumaiko; dziko la Aigupto lomwe silidzapulumuka.

43. Ndipo adzacita mwamphamvu ndi cuma ca golidi, ndi siliva, ndi zinthu zofunika zonse za Aigupto; Alubi ndi Akusi adzatsata mapazi ace.

44. Koma mbiri yocokera kum'mawa ndi kumpoto idzambvuta; nadzaturuka iye ndi ukali waukuru kupha ndi kuononga konse ambiri.

45. Ndipo adzamanga mahema a nyumba yacifumu yace pakati pa nyanja yamcere ndi phiri lopatulika lofunika; koma adzafikira cimariziro cace wopanda wina wakumthandiza.

Werengani mutu wathunthu Danieli 11