Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Danieli 1:13-21 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

13. Pamenepo mupenye maonekedwe athu ndi maonekedwe a anyamata akudya cakudya ca mfumu; ndi monga umo muonera, mucitire anyamata anu.

14. Ndipo anawamvera mau awa, nawayesa masiku khumi.

15. Atatha masiku khumiwo tsono, anaona kuti maonekedwe ao ndi kunenepa kwao anaposa anyamata onse adadyawo zakudya za mfumu.

16. Pamenepo kapitaoyo anacotsa cakudya cao ndi vinyo akadamwa, nawapatsa zomera m'nthaka.

17. Koma anyamata amene anai, Mulungu anawapatsa cidziwitso ndi luntha la m'mabuku ali onse, ndi nzeru; koma Danieli anali nalo luntha la m'masomphenya ndi maloto onse.

18. Atatha masiku inanenawo mfumu kuti alowe nao, mkulu wa adindo analowa nao pamaso pa Nebukadinezara.

19. Ndipo mfumu inalankhula nao, koma mwa iwo onse sanapezeka monga Danieli, Hananiya, Misaeli, ndi Azariya; naimirira iwo pamaso pa mfumu.

20. Ndipo m'mau ali onse anzeru ndi aluntha, amene mfumu inawafunsira, inawapeza akuposa alembi ndi openda onse m'ufumu wace wonse.

21. Nakhala moyo Danieli mpaka caka coyamba ca Koresi.

Werengani mutu wathunthu Danieli 1