Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 9:12-15 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. kuti alandire otsala a Edomu akhale colowa cao, ndi amitundu onse akuchedwa dzina langa, ati Yehova wakucita izi.

13. Taonani akudza masiku, ati Yehova, akud wolima adzapezana ndi wodula, ndi woponda mphesa adzapezana ndi wofesa, ndi mapiri adzakhetsa vinyo watsopano, ndi zitunda zonse zidzasungunuka.

14. Ndipo ndidzabwezanso undende wa anthu anga Israyeli, ndipo adzamanganso mabwinja, ndi kukhala m'menemo; nadzaoka minda ya mipesa nadzamwa vinyo wace, nadzalima minda ndi kudya zipatso zace.

15. Ndipo ndidzawaoka m'dziko mwao ndipo sadzazulidwanso m'dziko lao limene ndawapatsa, ati Yehova Mulungu wako.

Werengani mutu wathunthu Amosi 9