Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 7:14-17 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

14. Pamenepo Amosi anayankha, nati kwa Amaziya, Sindinali mneneri, kapena mwana wa mneneri, koma ndinali woweta ng'ombe, ndi wakuchera nkhuyu;

15. ndipo Yehova ananditenga ndirikutsata nkhosa, nati kwa ine Yehova, Muka, nenera kwa anthu anga Israyeli.

16. Cifukwa cace tsono, tamvera mau a Yehova, Iwe ukuti, Usamanenera cotsutsana ndi Israyeli, usadonthetsa mau akutsutsana ndi nyumba ya Isake;

17. cifukwa cace atero Yehova, Mkazi wako adzakhala wadama m'mudzi, ndi ana ako amuna ndi akazi adzagwa ndi lupanga, ndi dziko lako lidzagawanidwa ndi kuyesa cingwe, ndi iwe mwini udzafa m'dziko lodetsedwa; ndipo Israyeli adzatengedwadi ndende kucoka m'dziko lace.

Werengani mutu wathunthu Amosi 7