Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 7:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ambuye Yehova anandionetsa cotere; ndipo taonani, anaumba dzombe, poyamba kuphuka kwa maudzu a cibwereza; ndipo taonani, ndico cibwereza atawasengera mfumu.

2. Ndipo kunacitika m'mene lidatha kudya msipu wa dziko, ndinati, Ambuye Yehova, khululukiranitu Yakobo; adzakhala ciriri bwanji? popeza ndiye wamng'ono.

3. Ndipo Yehova anacileka. Sicidzacitika, ati Yehova.

4. Ambuye Yehova anandionetsa cotere; ndipo taonani, Ambuye Yehova anaitana kuti atsutse ndi moto; ndipo unanyambita cakudya cacikuru ukadanyambitanso dziko.

5. Pamenepo ndinati, Ambuye Yehova, Iekanitu; Yakobo adzakhala ciriri bwanji? pakuti ali wamng'ono.

6. Ndipo Yehova anacileka. Ici comwe sicidiacitika, ati Ambuye Yehova.

7. Anandionetsa cotere; ndipo taonani, Ambuye anaima pa khoma lomangiwda ndi cingwe colungamitsira ciriri; ndi cingwe colungamitsira ciriri m'dzanja lace.

Werengani mutu wathunthu Amosi 7