Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 6:7-14 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

7. Cifukwa cace tsono, adzatengedwa ndende ndi oyamba kutengedwa ndende; ndi phokoso la iwo odzithinula lidzapita.

8. Ambuye Yehova walumbira pali Iye mwini, ati Yehova Mulungu wa makamu, Ndinyansidwa nako kudzikuza kwa Yakobo, ndidana nazo nyumba zace zacifumu; m'mwemo ndidzapereka mudzi, ndi zonse ziri m'menemo.

9. Ndipo kudzacitika, mukatsala amuna khumi m'nyumba imodzi, adzafa.

10. Ndipo mbalewace wa munthu akamnyamula, ndiye womtentha, kuturutsa mafupa m'nyumba, nakati kwa iye ali m'kati mwa nyumbamo, Atsala wina nawe kodi? nakati, lai; pamenepo adzati, Khala cete; pakuti sitingachule dzina la Yehova.

11. Pakuti taonani, Yehova walamulira, nadzakantha nyumba yaikuru icite mpata, ndi nyumba yaing'ono icite mindala.

12. Kodi akavalo adzathamanga pathanthwe? kodi adzalimako ndi ng'ombe? pakuti mwasanduliza ciweruzo cikhale ndulu, ndi cipatso ca cilungamo cikhale civumulo;

13. inu okondwera naco copanda pace, ndi kuti, Kodi sitinadzilimbitsa tokha mwa mphamvu yathu yathu?

14. Pakuti taonani, ndidzakuutsirani mtundu wa anthu, nyumba ya Israyeli, ati Yehova Mulungu wa makamu; ndipo adzakupsinjani kuyambira polowera ku Hamati kufikira mtsinje wa kucidikha.

Werengani mutu wathunthu Amosi 6