Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 6:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tsoka osalabadirawo m'Ziyoni, ndi iwo okhazikika m'phiri la Samariya, ndiwo anthu omveka amtundu woposa wa anthu, amene nyumba ya Israyeli iwafikira!

2. Pitani ku Kaline, nimuone; kucokera komweko mupite ku Hamati wamkulu mutsikire ku Gati wa Afilisti; kodi awo ndi okoma koposa maufumu ano? kapena malire ao aposa malire anu?

3. Inu akutalikitsa tsiku loipa, ndi kusendeza pafupi mpando waciwawa;

4. ogona pa makama aminyanga, nadzithinula pa maguwa ao ogonapo, nadya ana a nkhosa a ku zoweta, ndi ana a ng'ombe ocoka pakati pa khola;

5. akungoyimba kutsata maliridwe a zeze, nadzilingiririra zoyimbira nazo Ingati Davide;

6. akumwera vinyo m'zipanda, nadzidzoza ndi mafuta abwino oposa, osagwidwa cisoni ndi kutyoka kwa Yosefe.

Werengani mutu wathunthu Amosi 6