Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 5:10-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

10. Iwo adana naye wodzudzula kucipata, nanyansidwa naye wolunjikitsa mau.

11. Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wace.

12. Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzocuruka, ndi macimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira cokometsera mlandu, akukankha osowa kucipata.

13. Cifukwa cace wocenierayo akhala cete nthawi yomweyo; pakuti ndiyo nthawi yoipa.

14. Funani cokoma, si coipa ai; kuti mukhale ndi moyo; motero Yehova Mulungu wamakamu adzakhala ndi inu, monga munena.

15. Danani naco coipa, nimukonde cokoma; nimukhazikitse ciweruzo kucipata; kapena Yehova Mulungu wa makamu adzacitira cifundo otsala a Yosefe.

16. Cifukwa cace atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! kalanga ine! nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.

17. Ndi m'minda yonse yamipesa mudzakhala kulira, pakuti ndipita pakati pako, ati Yehova.

18. Tsoka inu akufuna tsiku la Yehova! mudzapindulanji nalo tsiku la Yehova? ndilo mdima, si kuunika ai.

Werengani mutu wathunthu Amosi 5