Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 5:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israyeli inu.

2. Namwali wa Israyeli wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yace, palibe womuutsa.

3. Pakuti atero Ambuye Yehova, M'nyumba ya Israyeli, mudzi woturukamo cikwi cimodzi adzautsalira zana limodzi, ndi uwu woturukamo zana limodzi adzautsalira khumi.

4. Pakuti atero Yehova kwa nyumba ya Israyeli, Mundifunefune Ine, ndipo mudzakhala ndi moyo;

5. koma musamafuna Beteli, kapena kumalowa m'Giligala; musamapita ku Beereseba; pakuti Giligala adzalowadi m'ndende, ndi Beteli adzasanduka cabe.

6. Funani Yehova, ndipo mudzakhala ndi mayo; angabuke ngati moto m'nyumba ya Yosefe, ndipo unganyeke wopanda wakuzima m'Beteli;

7. inu osintha ciweruzo cikhale civumulo, nimugwetsa pansi cilungamo,

8. Iye wakulenga Nsangwe ndi Akamwiniatsatana, nasanduliza mdima wandiweyani ukhale m'mawa, nasanduliza usana ude ngati usiku, wakuitana madzi a m'nyanja, nawatsanulira pa dziko lapansi, dzina lace ndiye Yehova;

Werengani mutu wathunthu Amosi 5