Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 4:1-8 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tamverani mau awa, inu ng'ombe zazikazi za ku Basana, zokhala m'phiri la Samariya, zosautsa aumphawi, zopsinja osowa, zonena kwa ambuyao, Bwerani naco, timwe.

2. Ambuye Yehova walumbira pali ciyero cace, kuti taonani, adzakugwerani masiku akuti adzakucotsani ndi zokowera, ndi otsala anu ndi mbedza.

3. Ndipo mudzaturukira popasuka linga, yense m'tsogolo mwace, ndi kutayika ku Harimoni, ati Yehova.

4. Idzani ku Beteli, mudzalakwe ku Giligala, nimucurukitse zolakwa, nimubwere nazo nsembe zanu zophera m'mawa ndi m'mawa, magawo anu akhumi atapita masiku atatu atatu;

5. nimutenthe nsembe zolemekeza zacotupitsa, nimulalikire nsembe zaufulu, ndi kuzimveketsa; pakuti ici mucikonda, inu ana a Israyeli, ati Ambuye Yehova.

6. Ndipo ine ndakupatsaninso mano oyera m'midzi yanu yonse, ndi kusowa mkate m'malo mwanu monse; koma simunabwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

7. Ndipo Ine ndakumanani mvula, itatsala miyezi itatu isanafika nyengo yakukolola; ndipo ndinabvumbistira mudzi umodzi mvula, osabvumbitsira mudzi wina; munda wina unabvumbidwa mvula, ndi m'munda mosabvumbidwa mvula munafota.

8. M'mwemo midzi iwiri kapena itatu inayenda peyupeyu ku mudzi umodzi kukamwa madzi, koma sanakhuta; koma simunai bwerera kudza kwa Ine, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Amosi 4