Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

Amosi 3:1-10 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Tamverani mau awa akunenerani Yehova motsutsa, inu ana a Israyeli, kulinenera banja lonse ndinalikweza kuliturutsa m'dziko la Aigupto, ndi kuti,

2. Inu nokha ndinakudziwani mwa mabanja onse a pa dziko lapansi, m'mwemo ndidzakulangani cifukwa ca mphulupulu zanu zonse.

3. Kodi awiri adzayenda pamodzi asanapanganiranetu?

4. Kodi mkango udzabangula m'nkhalango wosakhala nayo nyama? Kodi msona wa mkango udzalira m'ngaka mwace usanagwire kanthu?

5. Kodi mbalame idzakodwa mumsampha pansi popanda msampha woichera? Kodi msampha ufamphuka pansi wosakola kanthu?

6. Kodi adzaomba lipenga m'mudzi osanieniemera anthu? Kodi coipa cidzagwera mudzi osacicita Yehova?

7. Pakuti Ambuye Yehova sadzacita kanthu osaulula cinsinsi cace kwa atumiki ace aneneri.

8. Mkango ukabangula, ndani amene saopa? Ambuye Yehova wanena, ndani amene sanenera?

9. Bukitsani ku nyumba zacifumu za Asidodi, ndi ku nyumba zacifumu za m'dziko la Aigupto, nimuziti, Sonkhanani pa mapiri a Samariya, ndipo penyani masokosero akuru m'menemo, ndi ozunzika m'kati mwace.

10. Pakuti sadziwa kucita zolungama, amene akundika zaciwawa ndi umbala m'nyumba zao zacifumu, ati Yehova.

Werengani mutu wathunthu Amosi 3