1. Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Moabu, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza anatentha mafupa a mfumu ya ku Edomu asanduke njereza;
2. koma ndidzatumiza moto pa Moabu, udzanyeketsa nyumba zacifumu za Kerioti; ndipo Moabu adzafa ndi phokoso, ndi kupfuula, ndi mau a lipenga;
3. ndipo ndidzalikha woweruza pakati pace, ndi kupha akalonga ace onse, ati Yehova.
4. Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Yuda, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza akaniza cilamulo ca Yehova, osasunga malemba ace; ndipo awalakwitsa mabodza ao amene makolo ao anawatsata;
5. koma ndidzatumiza moto pa Yuda, udzanyeketsa nyumba zacifumu za m'Yerusalemu.
6. Atero Yehova, Cifukwa ca zolakwa zitatu za Israyeli, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwace; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa cifukwa ca nsapato;
7. ndiwo amene aliralira pfumbi lapansi liri pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wace amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;
8. nagona pansi pa zopfunda za cikole ku maguwa a nsembe ali onse, ndi m'nyumba ya Mulungu wao akumwa vinyo wa iwo olipitsidwa.