Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 8:12-18 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

12. za Aaramu, za Amoabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleki, ndi zofunkha za Hadadezeri, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.

13. Ndipo Davide anamveketsa dzina lace pamene anabwera uko adakantha Aaramu m'cigwa ca mcere, ndiwo anthu zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.

14. Ndipo anaika maboma m'Edomu; m'dziko lonse la Edomu anaika maboma, ndipo Aedomu onse anasanduka anthu a Davide. Ndipo Yehova anasunga Davide kuli konse anamukako.

15. Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisrayeli onse, Davide naweruza ndi cilungamo mirandu ya anthu onse.

16. Ndipo Yoabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Josafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri,

17. ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi.

18. Ndipo Benaya mwana wa Jehoyada anayang'anira Akereti ndi Apeleti. Ndipo ana a Davide anali nduna zace.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 8