Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 7:23-29 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

23. Ndiponso mtundu uti wa pa dziko lapansi ufanana ndi anthu anu, ndiwo Israyeli, amene Mulungu anakadziombolera akhale anthu ace, ndi kuti limveke dzina lace, ndi kukucitirani zinthu zazikuru ndi kucitira dziko lanu zoopsa, pamaso pa anthu anu, amene munadziombolera kuwaturutsa ku dziko la Aigupto mwa amitundu ndi milungu yao?

24. Ndipo mwadzikhazikira anthu anu Aisrayeli, akhale anthu anu nthawi zonse, ndipo Inu Yehova munakhala Mulungu wao.

25. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, mau amene munalankhula za mnyamata wanu ndi za nyumba yace, muwalimbikitse ku nthawi zonse nimucite monga munalankhula.

26. Ndipo dzina lanu likulitsidwe ku nthawi zonse, kuti Yehova wit makamu ndiye Mulungu wa Israyeli, ndi nyumba ya mnyamata wanu Davide idzakhazikika pamaso panu.

27. Pakuti inu, Yehova wa makamu, Mulungu wa Israyeli, munaulula kwa mnyamata wanu kuti, Ndidzakumangira iwe nyumba; cifukwa cace mnyamata wanu analimbika mtima kupemphera pemphero gi kwa Inu.

28. Ndipo tsopano, Yehova Mulungu, Inu ndinu Mulungu, ndi mau anu adzakhala oona, ndipo Inu munaloniezana ndi mnyamata wanu kumcitira cabwino ici,

29. cifukwa cace tsono cikukomereni kudalitsa nyumba ya mnyamata wanu kuti ikhale pamaso panu cikhalire; pakuti Inu, Yehova Mulungu, munacinena; ndipo nyumba ya mnyamata wanu idalitsike ndi dalitso lanu ku nthawi zonse.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 7