Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 7:1-6 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo kunali pakukhala mfumuyo m'nyumba mwace, atampumulitsa Yehova pa adani ace onse omzungulira,

2. mfumuyo inanena ndi Natani mneneriyo, Onani ndirikukhala ine m'nyumba yamikungudza, koma likasa la Mulungu liri m'kati mwa nsaru zocinga.

3. Ndipo Natani anati kwa mfumuyo, Mukani mucite conse ciri mumtima mwanu, pakuti Yehova ali nanu,

4. Ndipo kunali usiku womwewo mau a Yehova anafika kwa Natani, kuti,

5. Kauze mtumiki wanga Davide, kuti, Atero Yehova, Kodi iwe udzandimangira nyumba yakuti ndikhalemo Ine?

6. pakuti sindinakhala m'nyumba kuyambira tsiku lija ndinaturutsa ana a Israyeli ku Aigupto kufikira lero lomwe, kama ndinayenda m'cihema ndi m'nyumba wamba.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 7