Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 23:1-7 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

1. Ndipo mau otsiriza a Davide ndi awa:—Atero Davide mwana wa Jese,Atero munthu wokwezedwa,Ndiye wodzozedwa wa Mulungu wa Yakobo,Ndi mwini masalmo wokoma wa Israyeli:

2. Mzimu wa Yehova unalankhula mwa ine,Ndi mau ace anali pa lilime langa,

3. Mulungu wa Israyeli anati,Thanthwe la Israyeli Gnalankhula ndi ine;Kudzakhala woweruza anthu molungama;Woweruza m'kuopa Mulungu.

4. Iye adzakhala ngati kuunika kwa m'mawa, poturuka dzuwa,M'mawa mopanda mitambo;Pamene msipu uphuka kuturuka pansi,Cifukwa ca kuwala koyera, italeka mvula.

5. Zoonadi nyumba yanga siikhala yotere ndi Mulungu;Koma iye anapangana ndi ine pangano losatha,Lolongosoka mwa zonse ndi losungika;Pakuti ici ndi cipulumutso canga conse, ndi kufuma kwanga konse,Kodi sadzacimeretsa?

6. Koma oipa onse adzakhala ngati minga yoyenera kuitaya,Pakuti siigwiridwa ndi dzanja;

7. Koma wakukhudza iyo adzikonzeratu citsulo ndi luti la mkondo;Ndipo idzatenthedwa konse ndi mota m'malo mwao.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 23