Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 22:6-19 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

6. Zingwe za kumanda zinandizingira;Misampha ya imfa inandifikira ine.

7. M'kusauka kwanga ndinaitana kwa Yehova,Inde ndinakuwira kwa Mulungu wanga;Ndipo Iye anamva mau anga ali m'kacisi wace,Ndi kulira kwanga kunafika ku makutuace.

8. Pomwepo dziko linagwedezeka ndi kunthunthumira.Maziko a dziko la kumwamba anasunthikaNagwedezeka, cifukwa iye anakwiya.

9. M'mphuno mwace munaturuka utsi,Ndi moto woturuka m'kamwa mwace unaononga;Makala anayaka nao.

10. Anaweramitsa miyambanso, natsika;Ndipo mdima wandiwe-yani unali pansi pa mapazi ace.

11. Ndipo iye anaberekeka pa Kerubi nauluka;Inde anaoneka pa mapiko a mphepo,

12. Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira iye,Kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yocindikira ya mlengalenga.

13. Ceza ca pamaso paceMakala a mota anayaka,

14. Yehova anagunda kumwamba;Ndipo Wam'mwambamwamba ananena mau ace.

15. Ndipo iye anatumiza mibvi, nawawaza;Mphezi, nawaopsa,

16. Pamenepo m'munsi mwa nyanja munaoneka,Maziko a dziko anaonekera poyera,Ndi mthonzo wa Yehova,Ndi mpumo wa mweya wa m'mphuno mwace.

17. Iye anatumiza kucokera kumwamba nanditenga;Iye ananditurutsa m'madzi akuru;

18. Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,Kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu,

19. Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga,

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 22