38. Ndinapitikitsa adani anga, ndi kuwaononga;Ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha.
39. Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka,Inde anagwa pansi pa mapazi anga.
40. Pakuti Inu munandimanga m'cuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; Munandigonjetsera akundiukira.
41. Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,Kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.
42. Anayang'ana iwo, koma panalibe wopulumutsa;Ngakhale kwa Yehova, koma iye sanawayankha.
43. Pomwepo ndinawasansantha asalale ngati pfumbi la padziko,Ndinawapondereza ngati dothi la m'makwalala.
44. Inunso munandipulumutsa ine pa kulimbana kwa anthu anga;Munandisunga ndikhale mutu wa amitundu;Anthu amene sindinawadziwa adzanditsumikira ine.
45. Alendo adzandigonjera ine,Pakumva za ine, adzandimbera pomwepo.
46. Alendo adzafota,Nadzabwera ndi kunthunthumira oturuka mokwiririka mwao.
47. Yehova ali ndi moyo; ndipo lidalitsike thanthwe langa;Ndipo akulitsidwe Mulungu wa thanthwe la cipulumutso canga;