27. Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;Ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
28. Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;Koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwacepetse.
29. Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;Ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.
30. Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;Ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.
31. Kunena za Mulungu, njira yace iri yangwiro;Mau a Yehova anayesedwa; iye ndiye cikopa kwa onse akukhulupirira iye.
32. Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?
33. Mulungu ndiye Gnga langa lamphamvu;Ndipo iye ayendetsa angwiro mu njira yace.
34. Iye asandutsa mapazi ace akunga mapazi a mbawala;Nandiika pa misanje yanga.
35. Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;Kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.
36. Ndiponso munandipatsa cikopa ca cipulumutso canu;Ndi kufatsa kwanu kunandikulitsa.
37. Munakulitsa kulunza kwanga pansi panga,Ndi mapazi anga sanaterereka.
38. Ndinapitikitsa adani anga, ndi kuwaononga;Ndiponso sindinabwerera mpaka nditawatha.
39. Ndinawatha ndi kuwapyoza, kuti sakhoza kuuka,Inde anagwa pansi pa mapazi anga.
40. Pakuti Inu munandimanga m'cuuno ndi mphamvu ya kunkhondo; Munandigonjetsera akundiukira.
41. Munatembenuzitsanso adani anga andipatse mbuyo,Kuti ndiwalikhe akudana ndi ine.