23. Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga;Ndipo za malemba ace, sindinawapambukira.
24. Ndinakhalanso wangwiro kwa iye,Ndipo ndinadzisunga kusacita kuipa kwanga.
25. Cifukwa cace Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;Monga mwa kuyera kwanga pamaso pace.
26. Ndi acifundo Inu mudzadzionetsa wacifundo,Ndi munthu wangwiro mudzadzionetsa wangwiro;
27. Ndi oyera mtima mudzadzionetsa woyera mtima;Ndi otsutsatsutsa mudzadzionetsa wopotoza.
28. Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa;Koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwacepetse.
29. Pakuti Inu ndinu nyali yanga, Yehova;Ndipo Yehova adzaunika mumdima mwanga.
30. Pakuti ndi Inu ndithamangira gulu;Ndi Mulungu wanga ndilumphira linga.
31. Kunena za Mulungu, njira yace iri yangwiro;Mau a Yehova anayesedwa; iye ndiye cikopa kwa onse akukhulupirira iye.
32. Pakuti Mulungu ndani, koma Yehova?Ndipo thanthwe ndani, koma Mulungu wathu?
33. Mulungu ndiye Gnga langa lamphamvu;Ndipo iye ayendetsa angwiro mu njira yace.
34. Iye asandutsa mapazi ace akunga mapazi a mbawala;Nandiika pa misanje yanga.
35. Iye aphunzitsa manja anga nkhondo;Kotero kuti manja anga alifula uta wamkuwa.