Chipangano Chakale

Chipangano Chatsopano

2 Samueli 22:18-25 Buku Lopatulika 1992 (BL92)

18. Iye anandipulumutsa kwa mdani wanga wamphamvu,Kwa iwo akudana ndi ine; pakuti anandiposa mphamvu,

19. Anandifikira ine tsiku la tsoka langa;Koma Yehova anali mcirikizo wanga,

20. Iye ananditurutsanso ku malo akuru;Iye anandipulumutsa, cifukwa akondwera ndi ine.

21. Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;Monga mwa kuvera kwa manja anga anandipatsa mphotho.

22. Pakuti ndinasunga njira za Yehova,Osapambukira koipa kusiya Mulungu wanga.

23. Pakuti maweruzo ace onse anali pamaso panga;Ndipo za malemba ace, sindinawapambukira.

24. Ndinakhalanso wangwiro kwa iye,Ndipo ndinadzisunga kusacita kuipa kwanga.

25. Cifukwa cace Yehova anandibwezera monga mwa colungama canga;Monga mwa kuyera kwanga pamaso pace.

Werengani mutu wathunthu 2 Samueli 22